PDF Archive

Easily share your PDF documents with your contacts, on the Web and Social Networks.

Share a file Manage my documents Convert Recover PDF Search Help ContactMpandamachokero Anthology by Bonwell Rodgers .pdf


Original filename: Mpandamachokero Anthology by Bonwell Rodgers.pdf
Title: Mpanda Machokero Series
Author: Bonwell Rodgers

This PDF 1.5 document has been generated by Microsoft® Word 2010, and has been sent on pdf-archive.com on 23/02/2017 at 11:26, from IP address 196.11.x.x. The current document download page has been viewed 384 times.
File size: 1.4 MB (360 pages).
Privacy: public file
Download original PDF file

Document preview


MPANDAMACHOKERO
ANTHOLOGY
By Bonwell Rodgers

Mawu Oyamba
M’bukuli muli nthano za ana. Nthano zina ndi zoti
zinalembedwa ndi akatswiri akale kwambiri ndipo
zinamasuliridwa n’kukonzedwa mwina ndi mwina,
pomwe zina ndi za kwathu konkuno ku Malawi.
Nthanozi ndi zazifupi koma zosangalatsa. Wolemba
bukuli anaona kuti anthu ambiri sakonda kuwerenga
nkhani zazitali. Choncho analemba nthano zazifupi
koma zomveka bwino. Nthanozi ndi zoti zikhoza
kugwiritsidwa ntchito pophunzitsa kusukulu,
powerengera ana komanso pocheza. Bukuli
lingathandizenso ana kuphunzira ukadaulo wopinda
komanso kuseweretsa mawu m’Chichewa.
Kuwonjezera apo, nthano zake ndi zokhathamira ndi
nsinjiro za chiyankhulo.

The Series of Rodgers Bounty Books [RBB]
Copyright © January 2015 by Bonwell Rodgers.
All rights reserved. No part of this publication may be reproduced or transmitted in any form or by any means, electronical or
mechanical, including photocopy, recording or any imformation storage and retrieval system, without permission in writing from the
owner.
Requests for permission should be mailed to: Bonwellrodgers91@gmail.com
Phone: 0881813953, 0881831435

1
Mpandamachokero Anthology

Nthano Zokhala ndi Maphunziro
“Tikhoza kuphunzira zambiri ngakhale kuchokera kwa
nyama zakutchire. Chilichonse chili ndi pokomera,
kungoti umafunika kufufuza mosamala kuti upaone
pokomerapo.”
—Anatero Lewis Carrol m’buku lake lakuti, Alice’s
Adventures in Wonderland

2
Mpandamachokero Anthology

Mbalame Yodzimva
M’nkhalango ina munali mbalame yokongola kwambiri
yomwe inkadya moto chifukwa cha kuyerekedwa
kwake. Dzina la mbalameyi linali Pikoko. Mbalameyi
inali yaphuzo chifukwa inkanyoza zinzake zomwe
zinali ndi nthenga zosaonetsa kugulu la anthu.
Inalinso yodzimva komanso yodzikuza zedi. Tsiku lina
mbalame zonse zitakhuta, zinapita pachitsime pomwe
zinkakamwa madzi. Mbalamezi zinkafunika kufola
pamzere kuti zikamwe madziwo. Ndiye chifukwa
chodziona kukongola, mbalame ija yotchedwa Pikoko
inangoyenda kupita kutsogolo n’kudutsa zinzake
zonse zomwe zinafika mofulumira. Mbalameyi
inkayenda monyang’wa ngati sipita kuchumbudzi, ili
palasu palasu palasu mpaka inakafika kutsogolo
kwenikweni. Anzake anaifunsa amvekere: “Chikatere?”
A Pikoko pomva izi anayamba kulavula mwano.
“Mulungutu enafe anatikondera! Kodi mumatichitira
nsanje eti?”
Mbalame zinzake zinadandaula kuti: “Chitsime
n’chimodzi m’mudzi muno, aliyense ayenera
kuchitiridwa mofanana kaya ali ndi nthenga zokongola
3
Mpandamachokero Anthology

kapena ayi, chilungamo chiziyenda ngati madzi!”
Koma mbalame ija inatuzula maso kwinaku
ikutokosera m’mano ndipo kenako inageyanso
chipongwe china cholama.
“Kodi mbalame zosasamba zikudzatani kuno? . . . Inu
a Khwangwala, ngati mumafuna kuchitiridwa zinthu
mofanana ndi enafe ingopitani kumanda! Ndipo
ndimadabwa kuti n’chifukwa chiyani nawonso manda
samaona kuti enafe tili ndi nthenga zokongola?
Tikazitambasula anthu amagwetsa zibwano zawo,
kudabwa kumeneko!”
Nang’omba atamva izi anatsutsa Pikoko. Kumenekotu
ndi kuyankhula kwa ntudzu komanso kogudukira.
Kukongoladi kwa mbalame n’kulinga utaiona
itatsegula pakamwa! Ndikuuzeni pano mosapsatira
mawu achikulire, kukongola kwa nthengaku
sikungakupangitseni kukhala wanzeru! Enafe
tinangoipa maonekedwewa, muntimamu si khalidwe
lake. Komanso tili ndi chikondi chopangitsa munthu
kuiwala kwawo!”
Mbalame zina zonse zinagwedezera mitu
povomerezana ndi a Nang’omba.
4
Mpandamachokero Anthology

“Mwayankhula bwino pamenepo a Nangomba!” Inatero
Nthiwatiwa. A Nthiwatiwa sanadziwe kuti zimene
anachitazo kunali kudzipalasira makala a moto,
ukadziotche weniweni. Pa nthawiyi n’kuti Pikoko
atapsa mtima, ukali ukutulukira mumphuno komanso
m’makutu, kwinaku atafutukura mapiko ake pofuna
kuwaonetsa anzakewo apo panagona kukongola
kwake. Kenako inakoka mtsonyo ikuyangana a
Nang’omba omwe anayandikana ndi a Nthiwatiwa.
Ndiyeno inayamba kulavula chichewa chitalichitali
chothiga ndi phuzo.
“Inu a Nang’omba ndinu chibenga. Nanunso a
Nthiwatiwa muli tiwa ngati nsungwi, zovala
zinakuthawani kalekale. Kodi simunamve kuti
munthu ukamafuna dzino lalikulu umafunika
kuutumba mulomo waukulu woti uvindikirire dzinolo?
Kutalika muli thobo, n’kumalephera kupeza zovala za
msinkhu wanu. Mumabwerekana zovala ndi mwana
wanu kapena? Mbalame zosasambanu mumatha
mawu kwabasi. Kaya n’kusowa khobili logulira
chinkhupule! Miyendo imeneyo ingapulumuke
mutakumana ndi khwekhwe kapena chimvwapula?
Mukamayenda mumangonunkha nkhwema
5
Mpandamachokero Anthology

kunkhwapa, simutisanzitsa inu? Kapena mumafuna
enafe tizichita nseru kuti chakudya m’malunjemu
chizitibwerera kukhosi! Umbombo wamtundu wanji
wofuna muzigalika nokha! Mukamayenda muli mimba
tiyetiye, nthenga zili yaviyavi, n’kumangooneka ngati
kamvuluvulu . . .”
Chipongwe chimenechi chinawafikapo a Nthiwatiwa
moti anayamba kuphulusika. Kenako anati:
“N’chifukwa chiyani anthu omwe muli pabwino
mumayankhula motumbwa?”
Koma a Pikoko anati: “Pajatu chilungamo
n’chipongwe! Kungoti enafe sitibisa mawu. Ena
akamatizolowera timangowamasura!”
Ndiyeno a Mkuta analowererapo n’kuuza a Pikoko
kuti, “Nafenso tikumasureni lero. Khalidwe lanu
limatinyansa, bolanso chimbudzi cha njovu kapena
fungo la dzila lowola.”
“Choka wouma mutu iwe!” Anatero a Pikoko.
“Namalenga ndiye anandinikha kukongolaku. Ngati
mumadziimba mlandu chifukwa cha kusaoneka bwino
kwanuko, mukawasumire makolo anu! Kodi
ndikanena chilungamo ndiye ndisanduke woipa?
6
Mpandamachokero Anthology

Osavula zigoba mwavalazo bwanji?”
Mbalame zonse zinadzuma ndipo ina yomwe inkamwa
madzi inatsamwa. Nthawi yomweyo Kadzidzi yemwe
n’kuti maso ake ali psuu chifukwa chosala tulo, zikope
zili thyo kuthyoka, anati: “A Pikokoo, palibetu
wangwiro padziko lapansi pano. Taonani miyendo
yanuyo!”
Mbalame zonse zinafa nawo nseko ndipo zina
zinangotsala pang’ono kukomoka chifukwa cha
chikhakhali. Zinkaseka miyendo ya a Pikoko yomwe
inali mbuu kutuwa ndipo inkangooneka ngati
zotokosera m’mano. Chifukwa cha manyazi, a Pikoko
anangosamukapo pachitsimepo, koma nyota
itangalula kukhosi.

Phunziro: Si bwino kukhala wodzikuza chifukwa
ngakhale utakhala ndi luso umakhala ndi penapake
pamene umalephera.

7
Mpandamachokero Anthology

Mafunso:
1.
N’chifukwa chiyani a Pikoko samafuna kukhala
pamzere?
2.
Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti a Pikoko
anali wodzikuza?
3.
Kodi pakati pa kukongola ndi khalidwe
labwino, chofunika kwambiri n’chiyani?
4.
Kodi tikuphunzirapo chiyani?

8
Mpandamachokero Anthology


Related documents


mpandamachokero anthology by bonwell rodgers
mpanda machokero series by bonwell rodgers finished book
niff programme as of 06 03 2018
intern blog my experience as a web graphic artist at inszoom
analytical philosophy
english document antonio aragao


Related keywords