Mpanda Machokero Series by Bonwell Rodgers [Finished Book] .pdf

File information


Original filename: Mpanda Machokero Series by Bonwell Rodgers [Finished Book].pdf
Title: Mpanda Machokero Series
Author: Bonwell Rodgers

This PDF 1.5 document has been generated by Microsoft® Word 2010, and has been sent on pdf-archive.com on 26/09/2016 at 15:27, from IP address 41.217.x.x. The current document download page has been viewed 533 times.
File size: 1.2 MB (136 pages).
Privacy: public file


Download original PDF file


Mpanda Machokero Series by Bonwell Rodgers [Finished Book].pdf (PDF, 1.2 MB)


Share on social networksLink to this file download pageDocument preview


MPANDA MACHOKERO
SERIES

Mawu Oyamba
M’bukuli muli nthano za ana. Nthano zina ndi zoti zinalembedwa
ndi akatswiri akale kwambiri ndipo zinamasuliridwa n’kukonzedwa
mwina ndi mwina, pomwe zina ndi za kwathu konkuno ku Malawi.
Nthanozi ndi zazifupi koma zosangalatsa. Wolemba bukuli anaona
kuti anthu ambiri sakonda kuwerenga nkhani zazitali. Choncho
analemba nthano zazifupi koma zomveka bwino. Nthanozi ndi zoti
zikhoza kugwiritsidwa ntchito pophunzitsa kusukulu, powerengera
ana komanso pocheza. Bukuli lingathandizenso ana kuphunzira
ukadaulo wopinda komanso kuseweretsa mawu m’Chichewa.
Kuwonjezera apo, nthano zake ndi zokhathamira ndi nsinjiro za
chiyankhulo.

Written by Bonwell Rodgers. Reproduction of this book is prohibited,
except with owner’s permission.
Email: Bonwellrodgers91@gmail.com
Phone: 0881813953, 0881831435
1
Mpanda Machokero Series

Zamkatimu
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba

001
007
008
009
010
011
012
014
015
017
018
019
020
021
023
024
025
026
027
028
029
030
031
032
033
035
036
037
037
038
040

Mawu Oyamba
Nkhandwe ya Mtima Wangati Kuseri kwa Mphika
Galu Apusitsidwa ndi Chithunzithunzi
Mkango Unatenga Zonse
Dokowe Apulumutsa Nkhandwe
Mpanda Machokero
Kusamvana Pakati pa Munthu ndi Njoka
Khoswe Wam’tauni ndi Khoswe Wakumudzi
Nkhandwe Ipusitsa Khwangwala
Mkango Udwala Mwakayakaya
Bulu Komanso Galu
Khoswe Apulumutsa Mkango
Namzeze Achenjeza Mbalame Zina
Achule Afuna Mfumu
Phokoso la Mapiri
Akalulu Akumana Ndi Mavuto
Ukakwera M’mwamba Usamatukwane Pansi
Pansi pa Mtima
Njoka Yopanda Pabwino
Ntchentche Yosimbwa
Nkhandwe Ichezera Dokowe
Nkhandwe Itola Chigoba Zokongola
Timba Anatengeka Ndi Mbalame
Kudzitama Kunaphetsa Chule
Ubwenzi wa Mkango ndi Kapolo
Mleme Uchenjera Pogona
Nkhani ya Mbawala ndi Mlenje
Njoka Ipsa Mtima
Mitengo Inadzipweteketsa
Galu Akumana ndi Nkhandwe
Ziwalo Ziukira Mimba
2

Mpanda Machokero Series

Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba

041
042
042
043
044
045
046
047
048
049
050
051
052
053
054
055
056
058
059
060
061
062
063
064
065
066
067
068
069
069
071
071
073
074

Mlimi Agwira Gwape Atabisala
Nkhandwe M’munda wa Mpesa
Ikakuthawa Imawawa Msuzi
Hatchi Akhaulitsa Mphoyo
Mbalame Yadyera
Chizolowezi Chimabala Mwano
Munthu Atsutsana ndi Mkango
Nyerere Yanzeru
Mtengo ndi Bango
Nkhandwe Yatulo
Nkhandwe Ivala Chikopa cha Nkhosa
Galu Apezeka Modyera Ng’ombe
Fano Lathabwa
Msodzi
Mnyamata Wabodza
Mpikisano wa Pakati pa Dzuwa ndi Mphepo
Mnyamata wa Zala Zazitali
Bambo Yemwe Anakwatira Mitala
Mayi ndi Nkhandwe
Msamuko wa Kamba
Nkhanu ndi Mwana Wake
Bulu Avala Chikopa cha Mkango
Nkhani ya Mabwenzi a Pamtima
Mapoto Awiri
Ng’ombe Zinayi ndi Mkango
Mneneri Wabodza
Msodzi Agwira Nsomba Yaing'ono
Munthu Wadyera Komanso Wansanje
Khwangwala Waludzu
Munthu Wam’nkhalango
Mazira Agolide
Mbalame Yoimba Mokoma
Nkhandwe, Nkhuku Komanso Galu
Munthu Wamanja Lende
3

Mpanda Machokero Series

Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba

075
076
077
078
079
080
081
083
084
085
086
087
089
090
091
092
093
094
095
096
097
098
099
100
101
103
104
105
106
107
109
110
111
112

Bambo ndi Mwana Wake Apita Kumsika
Munthu Woumira
Nkhandwe ndi Udzudzu
Nkhandwe Yopanda Mchira
kalulu wa Diso Limodzi
Msonkhano wa Makoswe
Mpikisano wa Kalulu ndi Kamba
Gogo Akumana ndi Imfa
Kalulu ndi Anzake Ambirimbiri
Mkango Ugwa M’chikondi
Kamtolo ka Mitengo
Mawu Omaliza a Mkango
Ubongo wa Mbawala
Nkhwazi Ibayidwa ndi Muvi
Kuwerengera Madzi a Mphutsi
Hatchi ndi Bulu
Woliza Lipenga
Katswiri Wolira Nyama Zosiyanasiyana
Nkhandwe ndi Mbuzi
Nsikidzi ndi Ana Ake
Nyani ndi Mwana Wake
Nkhuku ndi Mwala Wamtengo Wapatali
Khoswe ndi Msampha
Nkhani ya Kutha kwa Dziko
Nkhani ya Kalulu ndi Nkhandwe Yatulo
Anyamata Awiri Akumana ndi Munthu wokalamba
Chisoni Chinaphetsa Nkhwali
Chisoni Chinaphetsa Wosema Mitondo
Azimayi Anzeru
Mwana Wosamvera
Mwana Wamwano
Bambo ndi Mwana Wake
Kupulumukira Mkamwa mwa Mbuzi
Kodi Wochimwa Anali Ndani?
4

Mpanda Machokero Series

Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba
Tsamba

113
115
116
117
118
120
122
125
134

Mtsuko Wochucha Ndalama
Mphamvu Zobwereka
Anzeru Omwe Anali ndi Vuto Losaona
Nkhuku ndi Nkhunda
Mankhwala a Banja
Ndifera Manyazi Mkazi Wanga
Atambwali Sametana
Mutu Wodwala Kansire Adatema Kadzidzi
Angozo ndi Mwana Wawo

5
Mpanda Machokero Series

Nthano Zokhala ndi Maphunziro
“Tikhoza kuphunzira zambiri ngakhale kuchokera kwa nyama
zakutchire. Chilichonse chili ndi pokomera, kungoti umafunika
kufufuza mosamala kuti upaone pokomerapo.”
—Anatero Lewis Carrol m’buku lake lakuti, Alice’s Adventures in
Wonderland

6
Mpanda Machokero Series

Nkhandwe ya Mtima Wangati Kuseri kwa Mphika
Kalekalelo Nkhandwe inapita kukamwa madzi padziwe lina lomwe
linali pafupi ndi phiri. Itafika kumeneko inaima chakumtunda
n’kuyamba kupha ludzu. Itamwaza maso inaona Nkhosa, nayonso
ikumwa madzi kumunsi kwa dziwelo. Kenako inayamba kuganiza
kuti, “Ndikhozatu kutsuka mkamwa ndi kandiwo kameneka.
Nditangopeza chifukwa chabwino, ndikhoza kukaonetsa zakuda
ndithu.” Ndiyeno itadya mutu inayamba kuyankhula mwaukali kwa
Nkhosayo kuti, “N’chifukwa chiyani ukudetsa madzi amene
ndikumwa?” Nkhosayo inayankha kuti, “Ayi, si ine. Ngati madziwo
akubwera ali akuda kumeneko, vuto si ine ayi. Nokhanso mukuona
kuti madziwa akuchoka kumeneko n’kumabwera kuno.” Kenako
Nkhandwe ija inati, “Watero, chabwino, nanga n’chifukwa chiyani
unkanditukwana chaka chatha chija nditabwera kudzamwa madzi
kuno?” Nkhosayo inayankhanso kuti, “Si inenso ameneyo, inetu
ndili ndi miyezi isanu ndi umodzi wokha, moti nthawi imeneyo
ndinali ndisanabadwe.” Itamva zimenezi, Nkhandweyo inakwiya
kwambiri ndipo inati, “Ndilibe nazo ntchito zimenezo, ngati sunali
iweyo ndiye kuti anali bambo ako.” Itangonena zimenezi
inathamangira kunali Nkhosa kuja n’kuimbwandira, ndipo kenako
inaidya.
Phunziro: Munthu woipa sasowa chonamizira. Amachita chilichonse
kuti akwaniritse cholinga chake ngakhale kupha munthu kumene.
Mafunso
1. Kodi m’nthanoyi ndi nyama iti imene ili yoipa mtima?
N’chifukwa chiyani mwayankha choncho?
2. N’chifukwa chiyani mutu wa nkhaniyi ukuyerekeza mtima wa
nkhandwe ndi kuseri kwa mphika?
7
Mpanda Machokero Series

3. Perekani chitsanzo cha munthu woipa mtima yemwe anachitira
mnzake zankhanza, ngakhale kuti mnzakeyo anali wosalakwa.
4. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani?

Galu Apusitsidwa ndi Chithunzithunzi
Tsiku lina Galu anatola nyama ndipo anaipana n’kumapita nayo
kwawo kuti akaidye mwamtendere. Koma kuti akafike kwawo,
ankafunika kuwoloka mtsinje wina, ndipo kuti awoloke mtsinjewo
ankayenera kudutsa pa mlatho waung’ono. Galuyo atayamba
kuwoloka kudzera pamlathowo, anaona kuti m’madzi mukuoneka
chithunzithunzi cha Galu atanyamula nyama kukamwa kwake.
Ataona zimenezi, anaganiza kuti ameneyo ndi Galu wina. Chifukwa
chosakhutira ndi nyama yomwe anali nayo, Galuyo anaganiza
zolanda nyamayo kuti ikhalenso yake. Ndiyeno mwamphamvu,
analumphira m’madzi muja, kuti khuvuu! Koma atangotsegula
kukamwa kwake, nyama ananyamula ija inagwera m’madzi ndipo
anaisakasaka koma sanaipeze. Pamenepo m’pamene anazindikira
kuti Galu amaoneka mumtsinje uja chinali chithunzithunzi chake.
Phunziro: Musalole kutaya zonse zomwe muli nazo kuti mupeze
zinthu zomwe mulibe. Kumakhutira ndi zomwe muli nazo.
Mafunso
1. N’chifukwa chiyani Galuyu ankafunanso kulanda nyama ya
Galu amene ankamuona m’madzi, kodi anali ndi njala?
2. Kodi mukuganiza kuti Galu angachitedi zimenezi? N’chifukwa
chiyani mwayankha choncho?
3. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani?
8
Mpanda Machokero Series


Related documents


mpanda machokero series by bonwell rodgers finished book
mpandamachokero anthology by bonwell rodgers
the compilatoin of bonwell rodgers poems 1
record store day 2019   alle veroffentlichungen
peta jabatan 2014
paparan kemenaker

Link to this page


Permanent link

Use the permanent link to the download page to share your document on Facebook, Twitter, LinkedIn, or directly with a contact by e-Mail, Messenger, Whatsapp, Line..

Short link

Use the short link to share your document on Twitter or by text message (SMS)

HTML Code

Copy the following HTML code to share your document on a Website or Blog

QR Code

QR Code link to PDF file Mpanda Machokero Series by Bonwell Rodgers [Finished Book].pdf